Moto tiyatse moto yea
Moto tiyatse moto yea
Moto tiyatse moto yea
Moto
Yea uh
Malawi wangosanduka nkhalango
Tili mu tchire ndi ziyangoyango
Anthu nawo angosanduka mikango
Tokha tokha tingopatsana zilango
Tili mu tchire la umbombo ndi tsankho
Kuti zikuyendere kupondeleza anzako
Moyo wa lero wangosanduka battle
Umunthu unatha anthu anasanduka nsato
Za moyo wa udani tikukana toto
Ngati skeffa pali ponse tiyatsa chimoto
Komwe kuli tchireko nafe tili konko
Kum'mwera pakati mpakana kumpoto
Malawi yense ayake popanda potsala
Tivumbulutse chikondi pomwe chabisala
Tchire la kaduka lomaponyana miyala
Tiotche ndi moto wa chikondi mpaka litanyala
Kuli tchireko n'komwe kupita moto
Kuli tchireko n'komwe kupita moto
Pali ponse motowo uyake
Pali ponse motowo uyake yea yea
Oh oh oh oh
Motowo uyake Motowo uyake yea
Motowo uyake Motowo uyake yea
Yea yea yea yea yea
Yea yea yea yea yea
Malawi asagone tisatcholere
Nthawi ndi inoyo tizitolere
Chikondi moto udani ndi tchire
Malawi a chikondiwo akolele
Osamangokamba tiye zioneke
Mizu ya udani ndi moto inyeke
Ndi mgwilizano zonse zingatheke
Nde kusonkhezela moto wa ufulu tisaleke
Mphamvu ngati moto wa magetsi
Yea osaphweketsa machesi
Machesi ndi kamtengo kakang'ono
Koma kamaotcha nkhalango mukayatsa mapesi
Nde tiyeni nazo moto uyake
Tikusonkhezera nkhuni zake
Dzikoli likamudziwe tate
Za nsembe yake ndi chikondi chake
Kuli tchireko n'komwe kupita moto
Kuli tchireko n'komwe kupita moto
Pali ponse motowo uyake
Pali ponse motowo uyake yea yea yea
Oh oh oh oh
Motowo uyake motowo uyake yea
Motowo uyake motowo uyake yea
Yea yea yea yea yea
Yea yea yea yea yea
Motowo uyake Motowo uyake yea
Motowo uyake Motowo uyake yea
Yea yea yea yea yea
Yea yea yea yea yea